MAU A MTSOGOLERI OTSUTSA NYUMBA YAMALAMULO OLEMEKEZEKA DR KONDWANI NANKHUMWA, MP 49TH SESSION OF PARLIAMENT KUNYUMBA YAMALAMULO, LILONGWE 3 DECEMBER, 2021
Ndiyambe zoyankhula zanga pobweleza mau omwe mtsogoleri wadziko lino Dr Lazarus Chakwera anayankhula m’mbuyomu pamene anali paudindo monga wangawu. Iwo anati: “Pamene mafuta agalimoto akwera mtengo
Olemekezeka a sipika komanso aphungu anyumba ino,
Ndachitenga cha mtengo wapatali masana ano, kuyankhula kwa inu aphungu anzanga pamene tikutsekela zokambilana zamkumano wachi 49 wanyumba yamalamulo.
Koma poyamba ndithokoze aphungu onse anyumba ino potenga gawo pazokambilana zanyumbayi, izi ndi zomwe zapangitsa kuti zokambilanazi ziyende bwino komanso kupindulira anthu omwe timawayimilira pankhani zosiyanasiyana monga zandale,chitukuko komanso chuma chadziko lathu lino lokongola.
Ndikhala ndikulephera ntchito yanga ngati sinditchula komanso kulemekeza ntchito yabwino yomwe makomiti osiyanasiyana anyumba yamalamulo akugwira,pantchito yoonesesa kuti nthambi zaboma zikugwira ntchito zake moyenela.
Pachomwechi, ndafuna ndithokozenso utsogoleri wanyumba yamalamulo komanso boma poonetsetsa kuti makomitiwa akukumana pakakhala zinthu zofunikira kukambilana komanso kuyikapo upangili wawo.
Olemekeza a Sipika,
Uwu ndi nkumano wa aphungu otsiliza m’chaka chimenechi cha 2021, ndipo zokamba zanga zigona powunguza komanso kuwunikila msewu okumbika omwe dziko lino likudutsa pansi paulamuliro wamgwilizano wazipani za Tonse.
Olemekezeka a Sipika,
Ndiyambe zoyankhula zanga pobweleza mau omwe mtsogoleri wadziko lino Dr Lazarus Chakwera anayankhula m’mbuyomu pamene anali paudindo monga wangawu. Iwo anati: “Pamene mafuta agalimoto akwera mtengo, zomwe zapangisa katundu wazinthu zina kukweranso mtengo makamaka zakudya, ndipamene boma likukwezanso msonkho pazinthu zofunikira monga Mkaka komanso Bread.Kodichachitika ndi chani kulamulo loteteza anthu ogula la m’chaka cha 2013? Uku ndikulephera kwa utsogoleri”.
Olemekezeka a Sipika,
Iwo anapitilira ndikuyankhula kuti: “pamene zinthu zikupitilira kulowa pansi, ndipamene boma likuonjeza kugwilitsa ntchito misonkho ya anthu pazinthu zosafunikira monga kugula galimoto komanso kupanga hayala ndege ya mtsogoleri wadziko,zomwe zikuononga ndalama zankhaninkhani.
Akafunsidwa kuti kodi ndichifukwa chani mukuwononga ndalama pazinthu zopanda pake, iwoamakankhira izi kwa aphungu, ponena kuti ndinyumba yamalamulo yomwe imaloleza kagwilitsidwe ntchito kandalama. Koma chilungamo pankhaniyi,nyumba yamalamuliro imangololeza ndalama zomwe nyumba yachifumu yaboma ingagwilitse ntchito koma osati pazinthu zomwe nyumbayi ingagwilitsile ntchito ndalamazi.
Chisankho pogwilitsa ntchito ndalamazi pogulira galimoto komanso kupanga hayala ndege zimapangidwa ndi mtsogoleriyo payekha, ndipo zimaonetsa kulephera kwake kwautsogoleri.”
Olemekezeka a Sipika,
Dziko lapansi lili ndi njira zake zokukumbusila munthu pazinthu zomweunayankhupo m’mbuyomu.Munthu amene ndabwereza zomwe anayankhulayu ndi Dr Lazarus Chakwera, yemwe tsopano ndi mtsogoleri wa dziko la Malawi. Iwotu sizoti izi anayankhula pakale, ndiposachedwapapamene anali mtsogoleri wambali yotsutsa, asanalawe kukoma kwaulamuliro.
Pakadali panoali pampando onona pomwe akupanga zinthu zomwe zija zomwe amazifotokoza kuti ndikulephera kwa utsogolereli, ndipo pakadali pano zinthu zafika poyipisisa.
Panali chikhulupiliro komanso malonjezo ochuluka pamene boma lamgwilizano waTonse limalowa m’boma chaka chimodzi chapitacho. A Malawi analonjezedwa kuti azalembedwa ntchito, analonjezedwa boma lomvesela komanso lobwera mwansanga ndikukonza zinthu zikavuta.
A Malawianalonjezedwa zipangizo zaulimi zotsika mtengo; analonjezedwa ulamuliro odekha; kulumikizitsa magesi komanso madzi mwaulere kuphatikizilapo ma passport otsika mtengo. Sanalekeletu pompa a Malawi analonjezedwa ziphatso zoyendesera galimoto zosatha,komanso chinthu china analonjezedwa dziko lamkaka ndi uchila Kenani.
Olemekezeka a sipika
Lero zikuoneka kuti dziko lino lasokera ulendo waku Kenani uja, pamenezinthu zambiri sizikuyenda, koma mtsogoleri wadziko lino pamodzi ndi apabanja ake komanso anthu awazungulira ndiamene akusangalala.
M’malo mopanga mwayi wantchito 1 million, chuma cha dziko lino chalowelatu pansi,zomwe zapangisa kuti anthu ankhaninkhani achotsedwa ntchito momvesa chisoni.Mitengo yamafuta agalimoto yakwera zomwe zapangisanso kuti katundu wina ofunikira monga mafuta ophikira, Sopo, bread, machesi komanso mabandulo a internet kuti nawo akwere mtengo.
Nkhani yolumikiza madzi komanso magesi mwaulere ija sikukambidwanso, apa ndipamene boma lakweza mitengo yamadzi komanso magesi.
Nawo mtengo wafeteleza wakwera ndipo kuphatikizila apo, boma sizoti langokweza labwelesanso misonkho inapoonjezera ina yomwe inalipo kale, poonesesa kuti anthu mdziko muno akhaliretu mu umphawi.
Olemekezeka a Sipika,
Pano anthu ogwila ntchito m’boma komanso makampani ena omwe agwira ntchito zaboma, akulipiridwa mochedwa ndalama zawo kaamba kavuto la ndondomeko yomwe boma limagwiritsa ntchito polipira malipiro ndi ntchito zake zina ya Integrated Financial Management System (IFMIS).
Nduna yazachuma inadziwitsa nyumba ino chaka chatha, kuti ngati njira imodzi yopititsa patsogolo komanso kuteteza ndondomeko yachuma chaboma, boma kudzera kunthambi yolondoleza chuma chabomaya Accountant General, iyamba kugwilitsa ntchito ndondomeko yatsopano yolipilira malipiro ndi ntchito zina pa 1 July, 2020.
Koma ndizomvesa chisoni kuti IFMIS yatsopanoyi yabweresa mavuto ochuluka kusiyana ndi zabwino.Makampani omwe agwilira ntchito boma akulephera kulipilidwa ndalama zawo ndipo maunduna komanso nthambi zambiri zaboma akumalandira ndalama zawo mochedwa zomwe zikumakhuza ntchito zawo.
Olemekezeka a Sipika,
Ndalandila uthenga wina kuti munthu amene amaphunzitsa anthu zandondomeko yatsopano yaboma yolipilira anthu malipiro,wasiyila ntchitoyi panjira kaamba koti boma silimamulipira.
Pachifukwa ichi ndikupempha boma kuti lisiye kugwilitsa ntchito IFMIS yatsopanoyi kaamba koti ikhuza chuma cha dziko lino, m’malo mwake boma lipeze ndondomeko inayosavuta kugwilitsa ntchito komanso yodalilika.
Olemekezeka a Sipika,
Sizochita kubisanso kuti pakadali pano a Malawi akudusa m’mavuto azaonenei kaamba koti zinthu mdziko muno sizikuyenda.Chinthu chomvesa chisoni ndichakuti kulira kwawo sikukumveka ndipang’ono pomwe, kaamba koti aja amazitchula kuti ndi atsogoleri omvesera sakuonekenso.
Mtsogoleriyu watanganidwa ndi maulendo kupita m’malo komanso m’mayiko osiyanasiyana ndipo sakumvanso zamavuto a wanthu.
Pali mau oyela mu biyibulo, omweakuchokera mubukhu la Marko chaputala 10 vesi 45, ndipo akuti, “Pakuti ndithu, mwana wa munthu sanadza kutumikiridwa, koma kutumikira, ndi kupereka moyo wache dipo la anthu ambiri”.
A Chakwera pokhala mtumiki wamulungu amayenera kukhaka patsogolo kudziwa kuti iwondi mtumiki wa anthu osati bwana wawo. Iwo amayenelanso kutengela chitsanzo chomwe Yesu Khristu amachita, potumikila anthu muchowonadi ndi mtima onse.
Malingana ndi Chapter 3, ndime 12 mubuku lamalamulo adziko lino, pa (1) (a) amakamba kuti, “ ntchito zonse zamalamulo komanso ndale zopita kwa anthu a mdziko la Malawi,zikuyenera kupangidwa motsatira malamulo adziko pofuna kukwanilisa komanso kuteteza zofuna zawo.”.
Olemekezeka a Sipika,
Izi ndizodabwitsa kuti ngakhale Chakwera analumbila kuteteza malamulo adziko lino, koma iwo sakupanga chili chonse chokomela anthu omwe anawasankha kukhala paudindo omwe alipo tsiku lalero.
Akafunsidwa kuti kodi ndichifukwa chiyani mukapanga izi, iwo akumayankha kuti ino sinthawi yomawatumizira mauthenga kaamba koti sangakwanise kusamalira banja lawina aliyense.
Akumapitilira kunena kuti kusayenda bwino kwazinthu sikuno kokha ku Malawi komanso mayiko onse kuphatikizilapalo dziko la America lomwe nalolakhuzidwa ndi muliri wanthenda ya COVID 19.
A Chakwera akumapitilira kuwuza anthu kuti apilire ndikuvala zilimbe pamene dziko lino likudusa muzowawa.Koma funso lalikulu kumakhala lokuti, kodi boma likuchitapo chani pofuna kuthetsa mavuto omwe dziko lino likukumana nalo? Kodi mpaka tidikila dziko la America litipezele njira potengera kuti mavutowa ndi adziko lonse?
Olemekezeka a Sipika,
Ndinayankhula kale m’mbuyomu kuti ngati dziko sitingangokhala kumadikizila ziganizo zopangidwa kwina; Nafe tikuyenera kuyamba kumapanga ziganizo zathu ngati dziko loyima palokha. Ngakhale dziko la Malawi lili mgulu lamayiko, koma sitimangokamba kuti zinthu zikuvuta padziko lonse chifukwa izi munthu wamba ku Malawi sangazimvese.
Olemekezeka a Sipika,
Posachedwapa ndimatsatira zomwe mtsogoleri wadziko la Kenya a Uhuru Kenyatta amayankhula, kuti dziko la Kenya lachoka pa nambala 12 pandandanda wamayiko olemela muno mu Africa kufika panambala 6 mkatinkati mwa nthenda ya COVID 19. A Kenyatta anati izi zachitika kaamba kaulamuliro wabwino komanso kuyika chidwi pazomwe dziko lingakwanilitse kuchita munthawi yamavuto.
Mwanjira ina kudziwa zinthu zofunikira kupanga munthawi yamavuto, kumathandiza kupititsa patsogolo zinthu mdziko. Mwachitsanzo dziko la Kenya pakadali pano likupanga zipangizo zozitetezera kunthenda ya COVID 19 monga zotchinga pakamwa ndi mphuno zomwe zikugulitsidwa padziko lonse la pansi.
Komatu izi sizili choncho kuno ku Malawi, pamene chinthu chokhacho chabwino boma linaona munyengo ino ya COVID 19 ndikugwilitsa ntchito molakwika ndalama zomwe cholinga chake kunali kulimbana ndinthendayi.
Olemekezeka a Sipika,
Ndikufuna kutengelaponso mwayi kukumbusa boma lamgwirizano wa Tonse lomwe likutsogozedwa ndi Dr Lazarus Chakwera,kuti liyambe kukwinilitsa zinthu zomwe analonjeza kuti azapanga akazalowa m’boma ndipo asiye kunamizila nthenda ya COVID 19.
Mwina a Chakwera atchulanso kuvuta kwa zinthu padziko lonse kuti ndikomwe kukuwalephelesa kusintha nduna zawo patatha miyezi isanu ndi umodzi, komanso kulephera kuchitapo kanthu poyika munthu wina kulowa pampando omwe nduna ina yamwalira.
Mwina a Chakwera atchulanso kuvutakwa zinthu padziko lonse, kuti ndikomwe kukulephelesa boma lawo kupeleka mankhwala muzipatala za mdziko lino.
Mwina a Chakwera atchula kuvutakwa zinthu padziko lonse, kuti komwe kunapangisa kuti ndalama zogwilitsa ntchito polimbana ndi Covid 19 ziwonongedwe.
Mwinatu ndi Covid-19 yomwe yapangisa kuti pakhale mpungwempungwe ku bungwe la MERA komanso NOCMA pankhani yogula mafuta, yomwe anthu ena akunyumba yachifumu yaboma kuphatikizilapo mtsogoleri wadziko lino anatchulidwapo?
Kodi kulephera kuyika mfundo zakasintha kakwagwilidwe ntchito m’boma komanso kulephera kutulutsa lipoti lamomwe anthu agwilira ntchito yawo m’boma zikubweranso chifukwa chamavuto omwe akhuza dziko lonse lapansi?
Mwinadi ndimavuto apadziko lonse, omwe akupangisa kuti apolisi azithira utsi okhesa misonzi a Malawi omwe akumagwilitsa ntchito ufulu wawo kuchita zionetselo mdziko muno.
Kodi ndikuvutanso kwa zinthu padziko lonse komwe kwapangisa nkhokwe zosungila chimanga ku National Food Reserve Agency kuti kukhale pafupifupi kopanda kanthu, ndalama zogulira chimanga zitapititsidwa ku ndondomeko yogulira zipangizo zaulimi zotsika mtengo ya AIP yomwe tsogolo lake silikuoneka?
Mwinatu ndikuvuta kwazinthu padziko lonse komwe kukupangisa kuti bungwe logula mbewu kwa alimi la ADMARC lipitilire kulowa pansi, pomwe lafika polephera kugula chimanga olo ton imodzi yokha kuchokera kwa alimi?
Mwinatu ndikuvuta kwazinthu, pa dziko lonse komwe kwapangisa kuti dziko lino lizuzulidwe ndi mayiko ena padziko lonse kaamba kofuna kutsegula ofesi yaukazembe ku Jerusalem.
Olemekezeka a Sipika,
Ndili pankhani yomweyi yamdziko la Israel, bwanji mundilole kuti ndikhale nawo kumbali yagulu la Palestine Solidarity Movement – Malawi,podzuzula mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera komanso boma lake, pazaganizo lake lofuna kutsegula maofesi awukazembe ku Jerusalem zomwe ndizotsutsana ndi zomwe atsogoleri anakambilana kumkumanao wamayiko padziko lonse wa UNGA pa 21st December, 2017, kuti ganizo lopanga Jerusalem kukhala likulu ladziko la Israel silolondola.
Ndikufuna ndikhalenso mbali yagulu la Palestine Solidarity Movement – Malawi podzuzula boma ladziko lino,povota motsutsana ndi nthambi yowona maufulu a anthu la United Nations Human Rights Council,lomwe limafuna kufufuza pazamilandu yomwe dziko la Israel lipanga ku Gaza komwe maufulu a anthu wamba anapwanyidwa, kuphedwa kuphatikizilapo ana komanso amayi.
Olemekezeka a Sipika,
Chinthu chinanso ndikufuna ndiyankhulepo ndikhani yachileso chomwe chayikidwa kwa mayiko akumwera kwa Africa a SADC kuti sangalowe m’mayiko aku America komanso ku Ulaya kaamba kamtundu wina watsopano wa COVID 19yemwe wapezeka m’chigawo chamayikowa.
Kupezeka kwa mtundu wina wa COVID 19 yu pena ndi m’dalitso kwa a Malawi, kaamba koti tonse tikudziwa kuti tsopano mtsogoleri wathu saononganso misonkho ya anthu kuwuluka pandege kumapita m’maiko ena.
Pachilungamo chake, chiletsochi ndichopweteka ndipo chitiphunzitse kuyamba kuganiza moyima patokha pamomwe tingakonzere mavuto athu.
Uwutu ndi uthenga winanso opitakwa mtsogoleriwa wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera kuti maulendo awo opita kumayiko azungu alibe phindu chifukwa azungu wa akapanga chiganizo chimakhala chomwecho ndipo amaganizila kaye za anthu awo. Iwo samawerengelanso kuti apa pali wapampando wabungwe la SADC.
Olemekezeka a Sipika,
Posachedwapa ndamvaa President akulengeza kuti ayimisa maulendo awo onse pofuna kuwunikira mavuto a m’dziko muno. Kwainendikuti chiganizochi achipanga mochedwa. Kodi a President azindikila liti kutiali ndi ofesi? Azindikila liti kuti maulendo onse omwe akhala akuchita pakatipa bwenzi akutumizako nduna kapena mabwana mkubwa?
Ngakhale chiganizochi chili chabwino, koma ndikuganiza kuti iwo apanga izi atazindikira kuti maulendo omwe akhala akupanga akhala akuonongesa ndalama zochuluka za a Malawi, ndipo ndikuona kuti ndikwabwino kuti bwenzi anakangobwera poyera ndikufokozela izi.
Olemekezeka a Sipika
Komaliza,ndikufuna ndibweleze kunenanso mau ena omwe a Chakwera anayankhula, ndipo anati. “M’malawi aliyense kuyambila ku Chitipa mpaka Nsanje akudziwa kuti kulephera kwa dziko lino sichifukwa “chamavuto”, koma ndichifukwa chakulephera kwathu. Ndipo kulephera kumeneko ndichifukwa chakulephera kwa atsogoleri athu.”
Zomwe iwo amatanthauza apa ndizokuti zala zonse zimaloza kwa mtsogoleri wa dziko, ndipo okha anavomeleza kuti alephera kuyendesa dziko lino.
Olemekezeka a Sipika,
Ndikufuna ndigwirizane ndi mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera, kuti wakanika kupeleka ulamuliro omwe a Malawi amawufuna maaka panthawi yovuta monga iyi.
Asanakhale mtsogoleri wadziko lino,a Chakwera anayankhula kwaanthu ndipo anatsindika kuti ngati azalephere kulamulira bwino dziko lino muzaka ziwiri zoyambilira, azatula pansi udindo wawo.
Chinthu chokhacho chomwe a Chakwera angapange pakadali pano ndikutuladi pansi udindo wawo chifukwa zachita kuoneselatu kuti alephela, pamene angoyang’anira kuti zinthu zibwelera m’chimake zokha, zomwe ndizosatheka.
Olemekezeka a Sipika,
Potsiliza ndikufuna ndiwuze nyumba ino komanso a Malawi onse, kuti mbali yotsutsa sifooka poyima pachilungamo. Tipitilira kudzuzula bomangati silikugwila ntchito yokomela anthu mdziko muno chifukwa amenewo ndi amene anawayika pampando.
Tipitilira kugwila ntchito yathu mpakana tsika limene a Malawi onse azayambe kuyang’anidwa mofanana pamaso palamulo, komanso kupasidwa mwayi ofanana posatengera chipani chomwe akutsatila, khungu lawo, mtundu kapena chipembezo chomwe iwoali.
Ndathokoza kwambiri a Sipika komanso nonse olemekezeka,
Ndikuthokozeni kaamba kakumvesela kwanu ndipo Mulungu apitilire kudalitsa dziko la Malawi.